MA BILLION AKU MCP NDI DPP POKONZEKERA MA CONVENTION AWO

Поділитися
Вставка
  • Опубліковано 10 вер 2024
  • MA BILLION AKU MCP NDI DPP POKONZEKERA MA CONVENTION AWO
    Pamene zipani zikuluzikulu mdziko muno zili kalikiliki kuchita misonkhano yawo yayikulu ndi cholinga chosankha adindo ena amene ayendetse zipanizo mu zaka zisanu zikubwerazi ndikukonzekera masankho achaka cha mawa, zawululika tsopano kuti zipani za Malawi Congress (MCP) ndi Democratic Progressive (DPP) zigwiritsa ntchito ndalama zankhaninkani. Kumbali ya chipani cha MCP chimene msonkhano wake wawukulu wachitika kale mu sabata yangothayi, malipoti akuonetsa kuti chipanichi chinagwiritsa ntchito ndalama zokwana 1.5 billion kwacha kuti msonkhanowo utheke ndipo chipani cha DPP chimene chichititse msonkhano wake wawukulu pa 17 ndi pa 18 August 2024, chipanichi chigwiritsa ntchito ndalama zokwana 1 billion kwacha. Kodi zipani zimapeza bwanji ndalama zoterezi ndipo zimawunikidwa motani ngati palibe chinyengo chilichonse? Ili ndi funso limene anthu komanso mabungwe owona za ulamuliro wabwino akhala akumafunsa popeza palibe chipani chimene chimabwera poyera ndi kunena za komwe atenga ndalama zoterezi.

КОМЕНТАРІ • 4

  • @enerstmakochera3956
    @enerstmakochera3956 25 днів тому

    Thanks bro well clarifying

  • @FrancisStima-sc7zs
    @FrancisStima-sc7zs 25 днів тому +1

    DPP ipangabwanji chinyengo ilikunja kwaboma aaaaa

  • @user-io2uw2me9f
    @user-io2uw2me9f 24 дні тому

    Dpp ndi mcp onsewa ndi anthu akuba iyaaaa

  • @GideonMunthali
    @GideonMunthali 24 дні тому

    Nkhaniyi akuyankhulayu mutu wake sumugwila ntchito mwangozaza mamina okhawokha chifukwa tikayankhila za dpp ipanga bwanji chinyengo choba ndalama pomwe ili kunja kwa boma anakanena za mcp zinali zoveka bwinobwino